Yobu 3:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,Akudzimangira m'mabwinja;

15. Kapena pamodzi ndi akalonga eni ace a golidi,Odzaza nyumba zao ndi siliva;

16. Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zi;Ngati makanda osaona kuunika.

17. Apo oipa aleka kumabvuta;Ndi apo ofoka mphamvu akhala m'kupumula.

Yobu 3