Yobu 3:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pace, natemberera tsiku lace.

2. Nalankhula Yobu nati,

3. Litayike tsiku lobadwa ine,Ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.

4. Tsiku lija likhale mdima;Mulungu asalifunse kumwamba,Ndi kuunika kusaliwalire.

Yobu 3