Yobu 29:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Dalitso la iye akati atayike linandidzera,Ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauyimbitsa mokondwera.

14. Ndinabvala cilungamo, ndipo cinandibvala ine;Ciweruzo canga cinanga mwinjiro ndi nduwira.

15. Ndinali maso a akhungu,Ndi mapazi a otsimphina.

16. Ndinali atate wa waumphawi;Ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa.

17. Ndipo ndinatyola nsagwada ya wosalungama,Ndi kukwatula cogwidwa kumano kwace.

18. Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'cisa canga;Ndipo ndidzacurukitsa masiku anga ngati mcenga.

19. Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;Ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.

20. Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,Ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga.

21. Anthu anandimvera, nalindira,Nakhala cete, kuti ndiwapangire.

Yobu 29