5. Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya,Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.
6. Miyala yace ndiyo malo a safiro,Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.
7. Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.
8. Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.
9. Munthu atambasulira dzanja lace kumwala;Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.