Yobu 28:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Topazi wa Kusi sufanana nayo,Sailinganiza ndi golidi wolongosoka.

20. Koma nzeru ifuma kuti?Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?

21. Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,

22. Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.

23. Mulungu ndiye: azindikira njira yace,Ndiye adziwa pokhala pace.

24. Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,Naona pansi pa thambo ponse;

25. Pamene anaikira mphepo muyeso wace,Nayesera madzi miyeso;

26. Pakucitira mvula lamulo,Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27. Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;Anaikonza, naisanthula.

28. Koma kwa munthu anati,Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.

Yobu 28