Yobu 27:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.

7. Mdani wanga akhale ngati woipa,Ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.

8. Pakuti ciyembekezo ca wonyoza Mulungu nciani pomlikhatu Mulungu,Pomcotsera moyo wace?

9. Kodi Mulungu adzamvera kupfuula kwace, ikamdzera nsautso?

10. Kodi adzadzikondweretsa naze Wamphamvuyonse,Ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?

11. Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;Cokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzacibisa.

12. Taonani, inu nonse munaciona;Ndipo mugwidwa nazo zopanda pace cifukwa ninji?

13. Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,Ndi colowa ca akupsinja anzao acilandira kwa Wamphamvtiyonse.

14. Akacuruka ana ace, ndiko kucurukira lupanga,Ndi ana ace sadzakhuta cakudya.

15. Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,Ndi akazi ace amasiye sadzalira maliro.

16. Cinkana akundika ndalama ngati pfumbi,Ndi kukonzeratu zobvala ngati dothi;

17. Azikonzeretu, koma wolungama adzazibvala,Ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.

Yobu 27