Yobu 27:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Amanga nyumba yace ngati kadzoce,Ndi ngati wolindira amanga dindiro.

19. Agona pansi ali wacuma, koma saikidwa;Potsegula maso ace, wafa cikomo,

20. Zoopsa zimgwera ngati madzi;Nkuntho umtenga usiku.

21. Mphepo ya kum'mawa Imtenga, nacokaiye;Nimkankha acoke m'malo mwace.

22. Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osanlieka;Kuthawa akadathawa m'dzanja lace.

Yobu 27