5. Adafawo anjenjemeraPansi pa madzi ndi zokhalamo,
6. Kumanda kuli padagu pamaso pace,Ndi kucionongeko kusowa cophimbako,
7. Ayala kumpoto popanda kanthu, Nalenjeka dziko pacabe.
8. Amanga madzi m'mitambo yace yocindikira;Ndi mtambo sung'ambika pansi pace,
9. Acingira pa mpando wace wacifumu,Nayalapo mtambo wace.
10. Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.
11. Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.