13. Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,Sadziwa njira zace,Sasunga mayendedwe ace.
14. Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;Ndi usiku asanduka mbala.
15. Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira,Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;Nabvala cophimba pankhope pace.
16. Kuli mdima aboola nyumba,Usana adzitsekera,Osadziwa kuunika.
17. Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18. Atengedwa ngati coyandama pamadzi;Gawo lao litembereredwa padziko;Sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.