Yobu 24:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;Aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.

12. M'mudzi waukuru anthu abuula alinkufa;Ndi moyo wa iwo olasidwa upfuula;Koma Mulungu sasamalira coipaco.

13. Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,Sadziwa njira zace,Sasunga mayendedwe ace.

14. Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;Ndi usiku asanduka mbala.

15. Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira,Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;Nabvala cophimba pankhope pace.

16. Kuli mdima aboola nyumba,Usana adzitsekera,Osadziwa kuunika.

Yobu 24