7. Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.
8. Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;Kapena m'mbuyo sindimzindikira;
9. Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;Akabisala kulamanja, sindimuona,
10. Koma adziwa njira ndilowayi;Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.
11. Phazi langa lagwiratu moponda Iye,Ndasunga njira yace, wosapambukamo.
12. Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.