Yobu 22:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2. Kodi munthu apindulira Mulungu?Koma wanzeru angodzipindulira yekha.

3. Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama?Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

4. Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu,Cifukwa ca kumuopa kwako?

5. Zoipa zako sizicuruka kodi?Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi?

Yobu 22