Yobu 21:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao,Ndi ana ao pamaso pao,

9. Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha,Ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.

10. Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika;Ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.

11. Aturutsa makanda ao ngati gulu,Ndi ana ao amabvinabvina.

12. Ayimbira lingaka ndi zeze,Nakondwera pomveka citoliro.

Yobu 21