Yobu 21:30-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?Naturutsidwa tsiku la mkwiyo?

31. Adzamfotokozera ndani njira yace pamaso pace?Nadzamlipitsa ndani pa ici anacicita?

32. Potsiriza pace adzapita naye kumanda,Nadzadikira pamanda pace,

33. Zibuma za kucigwa zidzamkomera.Adzakoka anthu onse amtsate,Monga anamtsogolera osawerengeka.

Yobu 21