Yobu 21:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16. Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao;(Koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17. Ngati nyali za oipa zizimidwa kawiri kawiri?Ngati tsoka lao liwagwera?Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wace?

18. Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,Ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19. Mukuti, Mulungu asungira ana ace a munthu coipa cace,Ambwezere munthuyo kuti acidziwe.

20. Aone yekha cionongeko cace m'maso mwace,Namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21. Pakuti comsamalitsa nyumba yace nciani, atapita iye,Ciwerengo ca miyezi yace citadulidwa pakati?

22. Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru?Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.

23. Wina akufa, wabiriwiri,Ali cikhalire ndi cipumulire.

24. Mbale zace zidzala ndi mkaka;Ndi wongo wa m'mafupa ace uli momwe.

25. Koma mnzace akufa ali nao mtima wakuwawa,Osalawa cokoma konse.

Yobu 21