Yobu 21:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Atsekereza masiku ao ndi zokoma,Natsikira m'kamphindi kumanda.

14. Koma adati kwa Mulungu, Ticokereni;Pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15. Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16. Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao;(Koma uphungu wa oipa unditalikira.)

Yobu 21