Yobu 20:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Cinkana coipa cizuna m'kamwa mwace,Cinkana acibisa pansi pa lilime lace;

13. Cinkana acisunga, osacileka,Naoikhalitsa m'kamwa mwace;

14. Koma cakudya cace cidzasandulika m'matumbo mwace,Cidzakhala ndulu ya mphiri mkati mwace.

15. Anacimeza cuma koma adzacisanzanso;Mulungu adzaciturutsa m'mimba mwace.

16. Adzayamwa ndulu ya mphiri;Pakamwa pa njoka padzamupha.

17. Sadzapenyerera timitsinje,Toyenda nao uci ndi mafuta.

18. Cimene adagwiriraco nchito, adzacibweza, osacimeza;Sadzakondwera monga mwa zolemera zace adaziona.

19. Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi;Analanda nyumba mwaciwawa, imene sanaimanga.

20. Popeza sanadziwa kupumula m'kati mwace,Sadzalanditsa kanthu ka zofunika zace.

21. Sikunatsalira kanthu kosadya iye,Cifukwa cace zokoma zace sizidzakhalitsa.

22. Pomkwanira kudzala kwace adzakhala m'kusauka;Dzanja la yense wobvutika lidzamgwera,

23. Poti adzaze mimba yace,Mulungu adzamponyera mkwiyo wace waukali,Nadzambvumbitsira uwu pakudya iye.

24. Adzathawa cida cacitsulo,Ndi mubvi wa uta wamkuwa udzampyoza.

25. Auzula, nuturuka m'thupi mwace;Inde nsonga yonyezimira ituruka m'ndulu mwace;Zamgwera zoopsa.

Yobu 20