Yobu 19:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Anandibvula ulemerero wanga,Nandicotsera korona pamutu panga,

10. Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;Nacizula ciyembekezo canga ngati mtengo.

11. Wandiyatsiranso mkwiyo wace,Nandiyesera ngati wina wa adani ace.

Yobu 19