Yobu 19:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Yobu anayankha, nati,

2. Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,Ndi kundityolatyola nao mau?

3. Kakumi aka mwandicititsa manyazi;Mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.

4. Ndipo ngati ndalakwa ndithu,Kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.

5. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;

Yobu 19