Yobu 18:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti aponyedwa m'ukonde ndi mapazi ace,Namaponda pamatanda.

9. Msampha udzamgwira kucitende,Ndi khwekhwe lidzamkola.

10. Msampha woponda umbisikira pansi,Ndi msampha wa cipeto panjira.

11. Zoopetsa zidzamcititsa mantha monsemo,Nadzampitikitsa kumbuyo kwace.

Yobu 18