Yobu 15:28-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Adzakhala m'midzi yopasuka,M'nyumba zosakhalamo munthu,Zoti zisandulika muunda.

29. Sadzakhala wolemera, ndi cuma cace sicidzakhalitsa,Ndi zipatso zace sizidzacuruka padziko.

30. Sadzacoka mumdima;Lawi la moto lidzaumitsa nthambi zace;Ndipo adzacoka ndi mpumo wa m'kamwa mwace.

31. Asatame zopanda pace, kudzinyenga nazo;Pakuti zopanda pace zidzakhala combwezera cace.

32. Cidzacitika isanadze nthawi yace;Pakuti nthambi yace siidzaphuka.

33. Adzayoyoka zipatso zace zosapsa ngati mpesa,Nadzathothoka maluwa ace ngati mtengo wazitona.

34. Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala cumba,Ndi moto udzapsereza mahema a olandira cokometsera mlandu.

Yobu 15