Yobu 13:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Mvetsetsani mau anga,Ndi kunenetsa kwanga kumveke m'makutu mwanu.

18. Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;Ndidziwa kuti adzandimasula ndiri wolungama,

19. Ndaniyo adzatsutsana nane?Ndikakhala cete, ndidzapereka mzimu wanga.

20. Zinthu ziwiri zokha musandicitire,Pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu:

21. Mundicotsere dzanja lanu kutali,Ndi kuopsa kwanu kusandicititse mantha.

22. Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha;Kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu.

23. Mphulupulu zanga ndi zocimwa zanga ndi zingati?Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi cimo langa,

24. Mubisiranji nkhope yanu,Ndi kundiyesa mdani wanu?

Yobu 13