Yobu 12:22-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Abvumbulutsa zozama mumdima,Naturutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;

23. Acurukitsa amitundu, nawaononganso;Abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.

24. Awacotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,Nawasokeretsa m'cipululu copanda njira.

25. Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,Ndipo awayendetsa dzandi dzandi.

Yobu 12