Yobu 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2. Zoonadi inu ndinu anthu,Ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.

3. Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu.Sindingakucepereni;Ndani sadziwa zonga izi?

4. Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace,Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;Munthu wolungama wangwiro asekedwa.

Yobu 12