1. Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati,
2. Kodi mau ocurukawa sayenera kuwayankha?Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama?
3. Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa?Useka kodi, wopanda munthu wakukucititsapo manyazi?
4. Pakuti unena, Ciphunzitso canga ncoona,Ndipo ndiri woyera pamaso pako.