11. Munandibveka khungu ndi mnofu,Ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha,
12. Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima,Ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.
13. Koma izi munazibisa mumtima mwamu;Ndidziwa kuti ici muli naco:
14. Ndikacimwa mundipenya;Ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.
15. Ndikakhala woipa, tsoka ine;Ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutuwanga;Ndadzazidwa ndi manyazi, Koma penyani kuzunzika kwanga.
16. Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango;Mubweranso ndi kudzionetsera modabwiza kwa ine.
17. Mundikonzeranso mboni zonditsutsa,Ndi kundicurukitsira mkwiyo wanu;Nkhondo yobwereza-bwereza yandigwera.
18. Potero munandibadwitsa cifukwa ninji?Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.
19. Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala;Akadanditenga pobadwapo kumka nane kumanda.