Yobu 1:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PANALI munthu m'dziko la Uzi, dzina lace ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

2. Ndipo anabala ana amuna asanu ndi awiri, ndi ana akazi atatu.

3. Zoweta zacenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamila zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi aburu akazi mazana asanu, anchito ace omwe ndi ambiri; cotero munthuyu anaposa anthu onse'a kum'mawa.

4. Ndipo ana ace amuna anamuka kukacita madyerero m'nyumba ya yense pa tsiku lace; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao.

Yobu 1