Yesaya 57:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa cikumbutso cako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.

9. Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kucurukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutari; ndipo wadzicepetsa wekha kufikira kunsi ku manda.

10. Unatopa ndi njira yako yaitari; koma sunanene, Palibe ciyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; cifukwa cace sunalefuka.

11. Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kucita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhala cete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiopa Ine konse?

12. Ndidzaonetsa cilungamo cako ndi nchito zako sudzapindula nazo.

13. Pamene pakupfuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzacotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala naco colowa m'phiri langa lopatulika.

14. Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, cotsani cokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga.

Yesaya 57