11. ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.
12. Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutari ndi cilungamo;
13. ndiyandikizitsa cifupi cilungamo canga sicidzakhala patari, ndipo cipulumutso canga sicidzacedwa; ndipo ndidzaika cipulumutso m'Ziyoni, ca kwa Israyeli ulemerero wanga.