4. pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kucokera pakatipo, ndi mzimu wa ciweruziro, ndi mzimu wakutentha.
5. Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ace, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; cifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa cophimba.
6. Ndipo padzakhala cihema ca mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.