28. ndi mpweya wace uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi copetera ca cionongeko; ndi capakamwa calakwitsa, cidzakhala m'nsagwada za anthu.
29. Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi citoliro, kufikira ku phiri la Yehova, ku thanthwe la Israyeli,
30. Ndipo Yehova adzamveketsa mau ace a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lace, ndi mkwiyo wace waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
31. Pakuti ndi mau a Yehova Asuri adzatyokatyoka, ndi ndodo yace adzammenya.