15. Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israyeli, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala cete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
16. Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; cifukwa cace inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; cifukwa cace iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.
17. Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.
18. Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.