Yesaya 22:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa cigwa ca masomphenya.Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamacindwi?

2. Iwe amene wadzala ndi zimpfuu, mudzi waphokoso, mudzi wokondwa; ophedwa ako, sanaphedwa ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.

3. Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patari.

4. Comweco ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, cifukwa ca kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,

Yesaya 22