Yesaya 19:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Komanso iwo amene agwira nchito yakupala bwazi, ndi iwo amene aomba nsaru yoyera, adzakhala ndi manyazi.

10. Ndipo maziko ace adzasweka, onse amene agwira nchito yolipidwa adzabvutidwa mtima.

11. Akalonga a Zoani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?

12. Nanga tsopano anzeru ali kuti? akuuze iwe tsopano; adziwe cimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kucitira Aigupto.

13. Akalonga a Zoani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asoceretsa Aigupto, amene ali mwala wa pangondya wa mapfuko ace.

Yesaya 19