Yesaya 1:21-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.

22. Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.

23. Akuru ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera mirandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.

Yesaya 1