Yeremiya 9:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!

2. Ha, ndikadakhala ndi cigono ca anthu aulendo m'cipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwacokere, pakuti onse ali acigololo msonkhano wa anthu aciwembu.

Yeremiya 9