5. Ine ndidzanka kwa akuru, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi ciweruzo ca Mulungu wao. Koma awa anabvomerezana natyola gori, nadula zomangira zao.
6. Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.
7. Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.
8. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wace.