Yeremiya 48:40-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati ciombankhanga, adzamtambasulira Moabu mapiko ace.

41. Keroti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Moabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42. Ndipo Moabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, cifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

Yeremiya 48