3. Mau amveka kucokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukuru!
4. Moabu waonongedwa; ang'ono ace amveketsa kulira.
5. Pakuti adzakwera pa cikweza ca Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa citsiko ca Horonaimu amva kulira kowawa kwa cionongeko.
6. Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amarisece m'cipululu,
7. Pakuti, cifukwa wakhulupirira nchito zanu ndi cuma canu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.
8. Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.