Yeremiya 45:3-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Munati, Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova waonjezera cisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma,

4. Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, cimene ndamanga ndidzapasula, ndi cimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.

5. Kodi udzifunira wekha zinthu zazikuru? usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati cofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.

Yeremiya 45