Yeremiya 42:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.

18. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.

19. Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.

20. Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.

21. Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'cinthu ciri conse cimene Iye wanditumira ine naco kwa inu.

22. Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi caola, komwe mufuna kukakhalako.

Yeremiya 42