1. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yaciwiri, pamene iye anali citsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti,
2. Atero Yehova wocita zace, Yehova wolenga zace kuti azikhazikitse; dzina lace ndi Yehova:
3. Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikuru, ndi zolakika, zimene suzidziwa.