Yeremiya 30:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

9. koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene ndidzawaukitsira.

10. Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israyeli; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutari, ndi mbeu zako ku dziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala cete, palibe amene adzamuopsya.

11. Pakuti Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi ciweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosaparamula.

Yeremiya 30