6. Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.
7. Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zace; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.
8. Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzace, Yehova anatero nao mudzi waukuru uwu cifukwa ninji?
9. Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.