3. nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera malo ano coipa, cimene ali yense adzacimva, makutu ace adzacita woo.
4. Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;
5. namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, cimene sindinawauza, sindinacinena, sicinalowa m'mtima mwanga;