3. Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.
4. Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.
5. Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.
6. Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.
7. Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.
8. Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?