1. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za cirala.
2. Yuda alira, ndipo zipata zace zilefuka, zikhala pansi zobvekedwa ndi zakuda; mpfuu wa Yerusalemu wakwera.
3. Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.
4. Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.
5. Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.