17. Koma iwe ukwinde m'cuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.
18. Cifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wacitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akuru ace, ndi pa ansembe ace, ndi pa anthu a m'dziko.
19. Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; cifukwa Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.