Yakobo 3:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

2. Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

3. Koma ngati tiikiraakavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao Ionse,

4. Taonani, zombonso, zingakhale zazikuru zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kuli konse afuna wogwira tsigiro.

Yakobo 3