Rute 4:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndiponso Rute Mmoabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa colowa cace; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ace, ndi pa cipata ca malo ace; inu ndinu mboni lero lino.

11. Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;

12. ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamare anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

13. Momwemo Boazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wace; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.

Rute 4